Isaiah 23:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani dziko la Ababiloni, anthu ameneŵa palibenso, adatheratu. Aasiriya ndi amene asandutsa Tiro kuti akhale malo a zilombo. Adamanga nsanja zao zankhondo, adagumula malinga ake nasandutsa mzindawo bwinja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, dziko la Ababiloni; anthu awa sakhalanso; Asiriya analiika ilo likhale la zilombo zokhala m'chipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ake; nalipasula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onani dziko la Ababuloni, anthu amenewa tsopano atheratu! Asiriya asandutsa Turo kukhala malo a zirombo za ku chipululu; anamanga nsanja zawo za nkhondo, anagumula malinga ake ndipo anawasandutsa bwinja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, dziko la Akasidi; anthu awa sakhalanso; Asuri analiika ilo likhale la iwo okhala m'cipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ace; nalipasula.