Isaiah 23:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ikubwera pamene Tiro adzaiŵalika pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, imene ili ngati nthaŵi ya moyo wonse wa mfumu imodzi. Zitatha zaka zimenezo, Tiro adzakhala ngati mkazi wachiwerewere uja woimbidwa nyimbo ija yakuti:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Tiro adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, chidzakhala kwa Tiro monga m'nyimbo ya mkazi wadama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Turo adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, cidzakhala kwa Turo monga m'nyimbo ya mkazi wadama.