Isaiah 23:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri, Chauta adzachitapo kanthu pa Tiro. Mzindawo udzabwerera ku ganyu wake wakale uja. Ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu a dziko lonse lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Tiro, ndipo iye adzabwerera kumphotho yake, nadzachita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Turo, ndipo iye adzabwerera ku mphotho yace, nadzacita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.