Isaiah 23:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chita manyazi, iwe Sidoni, mzinda wamalinga wakunyanja, chifukwa nyanjayo yalankhula, yanena kuti, “Sindinamvepo zoŵaŵa za kubala, sindinaberekepo ana, ndipo sindinalerepo mwana, wamwamuna kapena wamkazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khala ndi manyazi, iwe Sidoni; chifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chita manyazi, iwe Sidimu pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti, “Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana; sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khala ndi manyazi, iwe Zidoni; cifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.