Isaiah 24:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi ndizo zimene zidzachitikire mtundu uli wonse wa pa dziko lapansi. Kudzakhala ngati khunkha la olivi ndi khunkha la mphesa, pamene kholola latha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake padzakhala chotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi ndiponso pakati pa mitundu ya anthu. Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa, kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace padzakhala cotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo waazitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ace.