Isaiah 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma otsala aja adzafuula ndi kuimba mokondwa. Akuzambwe adzatamanda ukulu wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amenewa adzakweza mau ao, nadzafuula; chifukwa cha chifumu cha Yehova, iwo adzafuula zolimba panyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe; anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amenewa adzakweza mau ao, nadzapfuula; cifukwa ca cifumu ca Yehova, iwo adzapfuula zolimba panyanja.