Isaiah 24:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku maiko akutali tilikumva nyimbo zotamanda, zoyamika Wolungama uja. Koma ine ndikuti: Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Onyenga akupitirizabe ndipo kunyenga kwao kukupitabe m'tsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda “Wolungamayo.” Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo, inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kucokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa ine! amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.