Isaiah 24:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense wothaŵa phokoso la zoopsazo adzagwa m'mbuna, ndipo wotuluka m'mbunamo adzakodwa mumsampha. Kudzagwa mvula yachigumula ndipo maziko onse a dziko adzagwedezeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wothawa phokoso la zoopsa adzagwa mʼdzenje; ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo adzakodwa ndi msampha. Zitseko zakumwamba zatsekulidwa, ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsya, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene aturuka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.