Isaiah 24:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense zidzamuchitikira mofanana: wansembe chimodzimodzi munthu wamba, antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna, antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi, wogula chimodzimodzi wogulitsa, wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa, okongola chimodzimodzi okongoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyace; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyace wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye.