Isaiah 24:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba; lalemedwa ndi machimo ake. Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lapansi lidzacita dzandi dzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati cilindo; ndi kulakwa kwace kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.