Isaiah 24:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwezi udzanyala, ndipo dzuŵa lidzachita manyazi, pakuti Chauta Wamphamvuzonse adzakhala mfumu. Adzalamulira pa phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi m'Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira; pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira caulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi m'Yerusalemu, ndi pamaso pa akuru akuru ace.