Isaiah 24:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Mulungu watemberera dziko lapansi, anthu am'dzikomo akuzunzika chifukwa cha machimo ao. Iwo amalizika, ndipo atsala ndi oŵerengeka okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake chitemberero chadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ochimwa, chifukwa chake okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi; anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo, iwo asakazika ndipo atsala ochepa okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace citemberero cadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ocimwa, cifukwa cace okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala.