Isaiah 25:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova ndinu Mulungu wanga; ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu, pakuti mwachita zodabwitsa zimene munakonzekeratu kalekale mokhulupirika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, cifukwa mwacita zinthu zodabwitsa, ngakhale: zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.