Isaiah 25:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzateteza phirili ndi dzanja lake, ndipo Amowabu adzaŵapondereza pomwe aliripo, monga momwe manyowa amaŵaponderezera m'dzenje.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu aponderezedwa padzala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake; ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo, ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Moabu adzaponderezedwa pansi m'malo ace, monga maudzu aponderezedwa padzala.