Isaiah 25:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amowabuwo adzayesa kutambasula manja ao monga amachitira munthu wosambira. Koma Chauta adzathetsa kudzitama kwao ndiponso luso la manja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye adzatambasula manja ake pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ake posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwake, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo, ngati mmene amachitira munthu wosambira. Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo ngakhale luso la manja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye adzatambasula manja ace pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ace posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwace, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ace.