Isaiah 25:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umathetsera kutentha, momwemonso mumaletsa nyimbo ya anthu ankhalwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga kutentha m'malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsa idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma. Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha, inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga kutentha m'malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsya idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuwa.