Isaiah 25:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa phiri ili la Ziyoni Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zokoma ndi la vinyo wabwino, phwando la nyama yonona ndi la vinyo amene wafikapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino. Phwando la nyama yonona ndi vinyo wabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'phiri limendi Yehova wa makamu adzakonzera anthu ace onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okha okha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.