Isaiah 25:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo iwo adzati, “Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu; ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa. Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira; tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndikusekereram'cipulumutso cace.