Isaiah 26:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo m'dziko la Yuda anthu adzaimba nyimbo iyi yakuti, “Tili ndi mzinda wamphamvu, Mulungu amautchinjiriza ndi zipupa ndi malinga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mudzi wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi. Tili ndi mzinda wolimba. Mulungu amawuteteza ndi zipupa ndi malinga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo adzayimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tiri ndi mudzi wolimba; Iye adzaikacipulumutso cikhale macemba ndi malinga.