Isaiah 26:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu woipa mukamchitira zabwino, saphunzira zachilungamo. Amachita zoipa m'dziko lachilungamoli, ndipo amalephera kuzindikira ukulu wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa, saphunzira chilungamo. Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo, ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira cilungamo; m'dziko la macitidwe oongoka, iye adzangocimwa, sadzaona cifumu ca Yehova.