Isaiah 26:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, mwasamula dzanja lanu kuti muŵalange, koma iwo sakuliwona. Anthuwo achite manyazi poona m'mene mumakondera anthu anu, ndipo moto umene mwasonkhera adani anu, uŵapsereze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange, koma iwo sakuliona dzanjalo. Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu; ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona cangu canu ca kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamariza adani anu.