Isaiah 26:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, mwatiliritsa monga momwe amalirira mkazi pa nthaŵi yobala mwana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yake yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kufuula m'zowawa zake; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu, ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yace yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kupfuula m'zowawa zace; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.