Isaiah 26:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife tidamva ululu, ndipo tidavutika ngati mkazi pa nthaŵi yobala mwana, koma sitidapindule kanthu. Sitidadzetse chipulumutso m'dziko lapansi pano, sitidabadwitse anthu atsopano pansi pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinachite chipulumutso chilichonse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana, koma sitinapindulepo kanthu, kapena kupulumutsa dziko lapansi; sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinacite cipulumutso ciri conse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.