Isaiah 26:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anu amene adafa adzakhalanso ndi moyo, matupi ao adzauka. Inu nonse amene muli m'manda, dzukani ndi kuimba mosangalala. Monga momwe mame amafeŵetsera pansi kutsitsimutsa zomera, momwemonso Chauta adzaukitsa anthu amene adafa kale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo; matupi awo adzadzuka. Iwo amene ali ku fumbi tsopano adzadzuka ndi kuyimba mosangalala. Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera, momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muyimbe, inu amene mukhala m'pfumbi; cifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzaturutsa mizimu.