Isaiah 26:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akubwera kuchokera kumene amakhala, akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo ao. Magazi okhetsedwa pa dziko lapansi adzaululuka, mitembo ya anthu ophedwa sidzabisikanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala; akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo. Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo; dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, Yehova adza kucokera ku malo ace kudzazonda okhala pa dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao; dziko lidzabvumbulutsa mwazi wace, ndipo silidzabvundikiranso ophedwa ace.