Isaiah 26:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye watsitsa anthu okhala pa malo okwera, waononga mzinda wamphamvu uja. Wagumula zipupa zake, ndipo waugwetsera pansi, pafumbi penipeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba, iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula, amagumula makoma ake ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa pfumbi.