Isaiah 26:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, ife timatsata njira ya malamulo anu, ndipo timakhulupirira Inu. Mtima wathu umangolakalaka kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama, ife timayembekezera Inu; mitima yathu imakhumba kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi cikumbukilo canu.