Isaiah 26:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku, mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani. Pamene muweruza dziko lapansi, anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse; nthawi yammawa ndimafunafuna Inu. Pamene muweruza dziko lapansi anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira cilungamo.