Isaiah 27:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo Chauta adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, kulanga Leviyatani, chinjoka chothaŵa chija, Leviyatani njoka yozeŵezeka, ndipo adzaphanso chilombo choopsa cham'nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo, Yehova ndi lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija, Leviyatani chinjoka chodzikulunga; adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lace lolimba ndi lalikuru ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yotamanga, ndi nangumi njoka yopindika-pindika; nadzapha cing'ona cimene ciri m'nyanja.