Isaiah 27:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wamalinga wasanduka bwinja. Wasanduka malo osiyidwa ndi oiŵalika ngati chipululu. Kumeneko kwasanduka busa la ziŵeto, ndipo ziŵeto zimapumulako ndi kumadya nthambi za mitengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mudzi wochingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati chipululu; mwanawang'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamaliza nthambi zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja, wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu; kumeneko amadyetselako ana angʼombe kumeneko zimapumulako ziweto ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mudzi wocingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati cipululu; mwana wa ng'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamariza nthambi zace.