Isaiah 27:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthambi za mitengoyo zikauma, amazithyola, ndipo akazi amazitola nazisandutsa nkhuni. Popeza kuti anthuŵa ndi osamvetsa, nchifukwa chake Mulungu amene adaŵalanga sadzaŵamvera chisoni, Iye amene adaŵapanga sadzaŵachitira chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni. Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru; kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni, ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ponyala nthambi zace zidzatyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; cifukwa cace Iye amene anawalenga sadzawacitira cisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.