Isaiah 27:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo Chauta mwini wake adzasonkhanitsa anthu ake mmodzimmodzi, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wace, kucokera madzi a nyanja, kufikira ku mtsinje wa Aigupto, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israyeli.