Isaiah 27:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati adani a anthu anga afuna kuti ndiŵatchinjirize, apangane nane za mtendere, ndithu apangane nane za mtendere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nachite nane mtendere; inde, achite nane mtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze; apangane nane za mtendere, ndithu, apangane nane za mtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nacite nane mtendere; inde, acite nane mtendere.