Isaiah 27:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaŵalanga pa kuŵapirikitsa ndi kuŵatumiza ku ukapolo. Adaŵachotsa ndi mpweya wake waukali, monga momwe kumachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kuvuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo, mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa, monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munalimbana naye pang'ono, pamene munamcotsa; wamcotsa iye kuomba kwace kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.