Isaiah 27:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero machimo a Israele adzakhululukidwa, ndipo adzaonetsa kulapa kwathunthu, akadzaphwanya miyala yonse ya maguwa achikunja ndi kuisandutsa fumbi. Maguwa ofukizapo lubani ndiponso mafano ofanizira Asera sadzaonekanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo. Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja, ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha. Sipadzapezekanso mafano a Asera kapena maguwa ofukiza lubani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, mwa ici coipa ca Yakobo cidzafafanizidwa, ndipo ici ndi cipatso conse cakucotsa cimo lace; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.