Isaiah 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efuremu! Tsoka kwa ulemerero wake umene wayamba kufota ngati duŵa, mzinda uja uli kumtunda kwa chigwa chachonde, umene amanyadira anthu oledzera vinyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu. Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa limene lili pa mutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'cigwa ca nthaka yabwino.