Isaiah 28:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta adzakuphunzitsani pang'onopang'ono, lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro, kuti mudzakhumudwe poyenda. Mudzapweteka, mudzakodwa mu msampha, ndipo adzakutengani ku ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova adzakuphunzitsani pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo, adzapweteka ndi kukodwa mu msampha ndipo adzakutengani ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.