Isaiah 28:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumanena kuti “Ife tidachita chipangano ndi imfa, ndipo manda satiwopsa ai. Chiwonongeko chikamadzafika, sichidzatikhudza konse. Inu mumakhulupirira mabodza ngati kothaŵira, ndipo mumadalira kunama kuti kukhale kopulumukira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa, ife tachita mgwirizano ndi manda. Pamene mliri woopsa ukadzafika sudzatikhudza ife, chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;