Isaiah 28:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano zimene akunena Ambuye Chauta nzakuti, “Ku Ziyoni ndikuika maziko a mwala wotsimikizika, mwala wapangodya wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu. Pamwalapo palembedwa kuti, ‘Wokhulupirira sadzagwedezeka.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: “Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri ngati maziko mu Ziyoni, mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu; munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wace wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.