Isaiah 28:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilungamo ndicho chidzakhala ngati chingwe choyesera maziko ake, ndipo ungwiro udzakhala ngati choongolera chake. Koma matalala adzaononga mabodza amene mumaŵakhulupirira, ndipo chigumula chidzamiza malo anu opulumukirapo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake, ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere; matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza, ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzayesa ciweruziro cingwe coongolera, ndi cilungamo cingwe colungamitsira ciriri; ndipo matalala adzacotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.