Isaiah 28:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipangano chimene mudachita ndi imfa chidzatha, kotero kuti manda adzayamba kukuwopsani. Chiwonongeko chikamadzafika, chidzakugonjetsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri woopsa udzakuponderezani pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa; mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa. Pakuti mliri woopsa udzafika, ndipo udzakugonjetsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kubvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalepereka; popita mliri woopsya udzakuponderezani pansi.