Isaiah 28:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi iliyonse imene chizidzaoneka, chizidzakukanthani. Chizidzafika m'maŵa mulimonse, usana ndi usiku. Tsono anthu akadzamvetsa uthenga umenewu, adzaopsedwa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ukadzangofika udzakutengani. Udzafika mmawa uliwonse, usiku ndi usana.” Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu adzaopsedwa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi zonse umapita, udzakutengani; cifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsya kokha, kumva mbiri yace.