Isaiah 28:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzamenya nkhondo monga adachitira ku phiri la Perazimu. Adzakalipa monga adachitira ku chigwa cha Gibiyoni. Adzachita zimene afuna, ngakhale kuti zidzaoneke ngati zachilendo. Adzatsiriza ntchito yake, ntchito yake yozizwitsayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni; adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo, ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'cigwa ca Gibeoni; kuti agwire nchito yace, nchito yace yacilendo, ndi kuti acite cocita cace, cocita cace cacilendo.