Isaiah 28:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono inu musanyozere mau ameneŵa. Mukatero, maunyolo anu adzakuthinani koposa. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, andiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzaononga dziko lonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano lekani kunyoza, mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri; Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za cionongeko cotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi.