Isaiah 28:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ulemerero wa mzinda uja umene uli ngati duŵa lokhala kumtunda kwa chigwa chachonde wayamba kufota. Udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa. Munthu akangoiwona, amaithyola ndi kuidya nthaŵi yomweyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja, udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa imene munthu akangoyiona amayithyola nthawi yokolola isanakwane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu pa cigwa ca nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kuca malimwe asanafike; polona wakupenya imeneyo, amaidya iri m'dzanja lace.