Isaiah 28:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo, akudzandira ndi zakumwa zaukali. Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali. Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo, ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali. Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya, amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo ndipo akusochera chifukwa cha mowa: ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo; akusochera chifukwa cha mowa, akudzandira pamene akuona masomphenya, kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi cakumwa caukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, adzandima popenya, napunthwa poweruza.