Isaiah 28:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akuti aphunzitse yani? Kodi uthengawo akuti afotokozere yani? Kodi ndife ana ongoleka kumene kuyamwa, kapena makanda ongoŵachotsa kumene kubere?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? Iwo amene aletsedwa kuyamwa, nachotsedwa pamawere?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani? Uthengawu akufuna kufotokozera yani? Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa, kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? iwo amene aletsedwa kuyamwa, nacotsedwa pamabere?