Isaiah 29:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa inu zinthu zilizonse zoziwona m'masomphenya zakhala zobisika ngati mau a m'buku lomatirira. Buku limenelo atapatsa wina wodziŵa kuŵerenga kuti aŵerenge, iye adzati, “Sindingathe, chifukwa choti nlomatidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, chifukwa lamatidwa ndi phula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, cifukwa lamatidwa ndi phula;