Isaiah 29:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye akuti, “Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo, ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso. Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutari ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;