Isaiah 29:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine ndidzapitiriza kuŵachitira zodabwitsa anthu amenewo. Nzeru za anthu ao anzeru zidzatha, ndipo kuchenjera kwa anthu ao ochenjera kudzazimirira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira kuwachitira ntchito zodabwitsa; nzeru za anthu anzeru zidzatha, luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace, taonani, ndidzacitanso mwa anthu awa nchito yodabwitsa, ngakhale nchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.